UNGA80: Uthenga Wanga kwa Atsogoleri, komanso kwa Achinyamata a ku Africa

Tili ku #UNGA80, nditaitanidwa ndi Youth Office ya United Nations โ€” pa chikondwerero cha zaka 30 za World Programme of Action for Youth (WPAY30).

Sabata ino ndayankhulapo pa ma event aakulu:

  • ku UNCDF pa Akazi Otsogolera mu Ntchito za Digital Financial Services;
  • kenako ndinayankhula nawo pa panel ya BBC Africa, limodzi ndi Assistant Secretary-General a UNDP, Ahunna Eziakonwa, ndi ma Minister a Digital Transformation ochokera ku Nigeria ndi Morocco, pokambirana za Tsogolo la Ntchito, Achinyamata, ndi AI;
  • ndipo anatipatsa mpata ocheza ndi atsogoleri a ku WIPO ร— ITU ร— ITC, monga ife achinyamata a bizinesi.

Ndinakhalanso wokondwa kwambiri kutsogolera Africa Regional Youth Forum pa Energy & Just Transition, komwe tinalankhula ndi atsogoleri a ku World Bank (Mission 300) ndi FAO mmene luso, mfundo za boma, ndi ndalama zingathandize achinyamata ku Africa kutsogolera kusintha kwa mphamvu kopanda tsankho komanso kokhazikika.

Kwa ine, WPAY30 yatikumbutsa kuti achinyamata si ogwiritsa ntchito malamulo okha โ€” koma ndi omwe akutenga nawo mbali pokonza mayankho kwa mavuto amene iwo akukumana nawo. Kudzera mu ntchito za ma kampani ndi ma organisation anga โ€” Bien Corporation, Q2 Corporation, Ntha Foundation, ndi Kwathu Kollective โ€” ndikunyadira kuthandiza achinyamata ku Africa kuphunzira kukonzekera osati nyengo zokha, koma zaka zambiri: kuyambira pa ndalama za digito ndi mโ€™bizinesi, kupita ku AI, ulimi, ndi mphamvu zokhazikika.

Ndinalandira mafunso angapo, pa nkhani ya mmene tikumvera pa zaka 80 za United Nations:

1. Kodi UN yapanga chiyani mโ€™zaka 80 zapitazi?

Mu zaka 80, UN yapanga nsanja imene mayiko amatha kukambirana ndi kuthetsa mikangano popanda nkhondo, ndipo yamanga maziko a mtendere, ufulu wa anthu, ndi chitukuko chokhazikika. Yatsogolera mayankho pa mavuto aumoyo ndi ngozi, yatsogolera nkhondo yolimbana ndi kusiyana kwa amuna ndi akazi, ndipo yapanga Sustainable Development Goals (SDGs) monga njira yogwirizana padziko lonse. Ku Africa makamaka, UN yathandiza kulimbitsa maboma, kuonjezera mwayi pa maphunziro ndi zaumoyo, komanso kulimbikitsa achinyamata ndi akazi.


2. Kodi UN imatanthauza chiyani kwa inu?

Ine ndiyamba moyo wanga wa ntchito ngati intern ku UN Women. Kwa ine, UN ndi chizindikiro cha chiyembekezo komanso malo wogwira ntchito. Ndi komwe achinyamata aku Africa ngati ine timatha kubweretsa malingaliro athu pa nsanja yapadziko lonse, kusinthana mfundo, komanso kupeza chithandizo chokulitsa mayankho kumayiko athu. UNDP Graduate Programme ndi imene idandibweretsa ku New York mu 2022, ndipo ma nsanja ngati UNGA amandipatsa mwayi wowonetsa zatsopano zomwe achinyamata akumanga. Zimandionetsa kuti mgwirizano wapadziko lonse ukhoza kukhala woyenda bwino ngati achinyamata ndi azimayi ali patebulo.


3. Kodi mgwirizano wapadziko lonse uli ndi phindu lanji kwa anthu wamba?

Mgwirizano wapadziko lonse umafotokoza moyo wa anthu tsiku ndi tsiku โ€” kuyambira katemera panthawi ya mliri, ndalama zokhazikika kuthana ndi kusintha kwa nyengo, mpaka malamulo a ndalama za digito omwe amalola mobile money ndi malonda a dziko lonse. Palibe dziko limodzi lomwe lingathetse mavuto monga njala, kusintha kwa nyengo, kapena kubwera kwa ndi AI lokha. Mgwirizano umabweretsa chidziwitso, chuma, ndi mtendere zomwe zimakhudza mwachindunji moyo wa anthu, ngakhale nthawi zina sakuona momwe mgwirizanowo umafikirira.


4. Uthenga wanu kwa atsogoleri a padziko lonse ndi uti?

Atsogoleri apeleke ndalama ndi kuyika chikhulupiriro pa zatsopano za achinyamata ndi njira zolinga za nthawi yayitali. Zaka zikubwerazi zidzatsogoleredwa ndi AI, kusintha kwa nyengo, ndi njira zachuma zatsopano โ€” koma mfundo ndi ndalama zimabwera mochedwa. Pitirizani kupanga zolinga zopitilira nthawi ya zisankho; pangani zinthu za mibadwo. Khalani ndi chidaliro kuti achinyamata si ogwiritsa ntchito chabe koma ndi okonza mayankho. Pangani malo omwe achinyamata aku Africa angathetse mavuto monga kuwonongeka kwa chakudya, kusowa kwa mphamvu, ndi kusapezeka kwa digito โ€” ndikupeza njira zokulitsira padziko lonse. Kumbukirani: mgwirizano wopanda kugwira ntchito limodzi sudzatibweretsa tsogolo limene tikufuna.

Achinyamata ku Africa amapanga 60% ya anthu onse, ndipo ndife okonzeka kupititsa dziko lathu patsogolo.


Read my Published Books:

If youโ€™d like to go deeper into my journey โ€” from Malawi, through the United Nations to Microsoft, you can find it in my books:

Get a snippet of my upcoming books:

CONNECT WITH NTHANDA ONLINE:

Learn more about Ms. Manduwi

About the Author

Related Posts

Discover more from By Nthanda Manduwi

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading